John 20:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Mariya wa Magadala mamawa, kusanayambe kuca, kumanda, napenya mwala wocotsedwa kumanda.