John 20:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mariya analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama cisuzumirire kumanda;