John 21:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ananena nayenso kaciwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.