John 21:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'cuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzaturutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.