John 21:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simoni Petro adaŵauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakaloŵa m'chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simoni Petro ananena nao, ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anaturuka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.