John 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti timalankhula zimene tikuzidziŵa, ndipo timachitira umboni zimene tidaziwona, koma inu simukukhulupirira mau athuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni wathu simuulandira.