John 3:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziŵika kuti wazichita momvera Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.