John 3:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzace wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukuru cifukwa ca mau a mkwatiyo; cifukwa cace cimwemwe canga cimene cakwanira.