John 4:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.