John 4:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “Zakhala bwanji?” Kapena kuti, “Bwanji mukulankhula naye?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamenepo anadza ophunzira ace; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna ciani? kapena, mulankhula naye ciani?