John 4:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace pamene Asamariya anadza kwa iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.