John 4:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira popeza kuti eniakewo nawonso adaapita ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Paska, ndipo adaaona zonse zimene Yesu adaachita pachikondwereropo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita m'Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace pamene anadza ku Galileya, Agalileva anamlandira iye, atakaona zonse zimene anazicita m'Yerusalemu paphwando; pakuti iwonso ananka kuphwando.