John 4:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa njira adakumana ndi antchito ake, ndipo iwo adamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ake anakomana naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ace anakomana, naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.