John 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mai wachisamariya uja adayankha nati, “Inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakutitu Ayuda sayenderana ndi Asamariya.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya),