John 5:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.