John 5:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti Atate amakonda Mwana, namuwonetsa zonse zimene Iwo akuchita. Atate adzamuwonetsanso ntchito zoposa zimenezi, kuti inu muzizwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azicita yekha: ndipo adzamuonetsa nchito zoposa izi, kuti mukazizwe,