John 5:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.