John 5:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.