John 5:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimaweruza monga momwe Atate amandiwuzira. Ndipo ndimaweruza molungama, popeza kuti sinditsata zimene ndifuna Ineyo, koma zimene afuna Atate amene adandituma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindikhoza kucita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; cifukwa kuti sinditsata cifuniro canga, koma cifuniro ca Iye ondituma Ine.