John 5:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane. Atate adandipatsa ntchito zimene ndiyenera kuzichita, ndipo ntchito ndikuchitazi zikutsimikiza kuti Atate ndiwo adandituma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.