John 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wodwalayo adati, “Ambuye, ndilibe munthu wondiloŵetsa m'dziŵemu madzi akavundulidwa. Ndikati ndiloŵemo, wina waloŵa kale.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndilibe wondiviika ine m'thamanda, paliponse madzi avundulidwa; koma m'mene ndilinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndiribe wondibvika ine m'thamanda, pali ponse madzi abvundulidwa; koma m'mene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.