John 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaadziŵa kuti anthuwo ankati adzamgwire ndi kumlonga ufumu. Motero adaŵachokera nakakweranso m'phiri payekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge ufumu, anacokanso kunka kuphiri pa yekha.