John 6:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake khamu la anthu limene lidaatsalira ku tsidya lija la nyanja, lidaadziŵa kuti chombo chinalipo chimodzi chokha. Anthuwo adaadziŵanso kuti Yesu sadaloŵe m'chombomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzira akewo anali atapita okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mawa mwace khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa yina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowa pamodzi ndi akuphunzira ace m'ngalawamo, koma akuphunzira ace adacoka pa okha;