John 6:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khamu lija lidaona kuti Yesu kulibe, ophunzira ake omwe kulibenso. Tsono anthu onsewo adaloŵa m'zombo zija, napita ku Kapernao kunka nafunafuna Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.