John 6:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Kunena zoona, inu mukundifuna osati chifukwa mudazimvetsa zizindikiro zozizwitsa zija ai, koma chifukwa mudadya chakudya chija mpaka kukhuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si cifukwa munaona zizindikilo, koma cifukwa munadya mkate, nimunakhuta.