John 6:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gwirani nchito si cifukwa ca cakudya cimene citayika koma ca cakudya cimene citsalira ku moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera cizindikilo.