John 6:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo ankanena kuti, “Kodi ameneyu si Yesu, mwana wa Yosefe uja? Bambo wake ndi mai wake suja tikuŵadziŵa? Nanga tsono anganene bwanji kuti, ‘Ndidatsika kuchokera Kumwamba?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wace ndi amai wace tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?