John 6:53 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinenandi inu, 10 Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wace, mulibe moyo mwa inu nokha.