John 6:71 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankanena Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote. Ngakhale anali mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, koma ndiye amene analikudzapereka Yesu kwa adani ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma adanena za Yudase, mwana wa Simoni Isikariote, pakuti iye ndiye amene akampereka iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.