John 7:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amangolankhula zakezake, amadzifunira yekha ulemu. Koma yemwe amafunira ulemu amene adamtuma, ameneyo ndiye woona, ndipo mumtima mwake mulibe chinyengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama.