John 7:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adakulamulani kuti muziwumbala ana anu aamuna (ngakhale mwambowo si wochokera kwa Mose koma kwa makolo); ndipo inu mumaumbala mwana wamwamuna ngakhale mpa tsiku la Sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inu mdulidwe (si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici Mose, anakupatsani inu mdulidwe (si kuti ucokera kwa Mose, koma kwa, makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.