John 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanayo mumamuumbala pa Sabata, kuwopa kuti Lamulo la Mose lingaphwanyidwe. Bwanji mukuipidwa nane chifukwa ndinachiritsa munthu kwathunthu pa tsiku la Sabata?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, cifukwa ndamciritsadi munthu tsiku la Sabata?