John 7:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, adalankhula mokweza mau kuti, “Ine mukundidziŵa, ndipo kumene ndidachokera mukudziŵakonso. Koma sindidabwere mwa kufuna kwanga ai. Atate amene ali wokhulupirika ndiwo adandituma. Inu simukuŵadziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yesu anafuula m'Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.