John 7:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afarisi adamva manong'onong'o a chikhamu cha anthu okamba za Yesu. Tsono iwo pamodzi ndi akulu a ansembe adatuma asilikali a ku Nyumba ya Mulungu kuti akamgwire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.