John 7:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo akulu a Ayudawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi iyeyu afuna kupita kuti kumene ife sitingakampeze? Kodi kapena akufuna kupita kwa anzathu amene adabalalikira kwa anthu a mitundu ina? Monga nkuti afuna kukaphunzitsa anthu akunja?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene?