John 7:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja adabwerera kwa akulu a ansembe ndi kwa Afarisi aja. Iwo adafunsa asilikaliwo kuti, “Bwanji simudabwere naye?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga Iye bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji?