John 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adati, “Ngakhale ndikudzichitira ndekha umboni, komabe umboni wangawo ngwoona, pakuti ndikudziŵa kumene ndidachokera, ndiponso kumene ndikupita. Koma inu simukudziŵa kumene ndidachokera, kapenanso kumene ndikupita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndicita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; cifukwa ndidziwa kumene ndinacokera ndi kumene ndimukako; koma e inu, simudziwa kumene ndicokera, ndi kumene ndimukako.