John 8:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo iwo adamufunsa kuti, “Atate akowo ali kuti?” Yesu adati, “Ine simundidziŵa, Atate anganso simuŵadziŵa. Mukadandidziŵa, bwenzi mutaŵadziŵanso Atate anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?” Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ananena ndi iye, Ali kuti Atate, wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukada-dziwanso Atate wanga.