John 8:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adanena mau ameneŵa pamene ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, m'chipinda cholandiriramo zopereka za anthu. Panalibe amene adamgwira, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa m'Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau awa analankhula m'nyumba ya cuma ca Mulungu pophunzitsa m'Kacisi; ndipo palibe munthu anamgwira iye, pakuti nthawi yace siinafike.