John 8:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Ayuda adati, “Kodi kapena akufuna kukadzipha, umo akunena kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ayuda ananena, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?