John 8:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili ndi zambiri zoti ndinene za inu, ndiponso zoti ndikutsutsireni. Koma amene adandituma ngwoona, ndipo ndimauza anthu a pansi pano zimene Iyeyo adandiwuza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiri nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa iye, zomwezo ndilankhuia kwa dziko lapansi.