John 8:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
5 Inu muli ocokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zace za atate wanu mufuna kucita. Iyeyu anali wambanda kuyambira paciyambi, ndipo sanaima m'coonadi, pakuti mwa iye mulibe coonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wace; pakuti ali wabodza, ndi atate wace wa bodza.