John 8:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayudawo adamuuza kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa. Abrahamu adamwalira, aneneri nawonso adamwalira. Ndiye Iwe ukuti, ‘Munthu akamvera mau anga sadzafa konse.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.