John 8:55 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu simudaŵadziŵe, koma Ine ndimaŵadziŵa, mwakuti ndikadati sindiŵadziŵa ndikadakhala wonama ngati inuyo. Koma ndimaŵadziŵa, ndipo ndimamvera mau ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo inu simunamdziwa Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo 12 inu simunamdziwa iye; koma Ine ndimdziwa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama cimodzimodzi inu; koma ndimdziwa iye, ndipo ndisunga mau ace.