John 8:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaamufunsa funsoli kuti amuyese ndi kumpeza chifukwa. Koma Yesu adaŵerama, nayamba kulemba pansi ndi chala chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye. Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ici ananena kuti amuyese iye, kuti akhale naco comneneza iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi cala cace.