John 8:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaŵeramuka naŵauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala,