John 9:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?” Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.