John 9:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ayuda sanakhulupirira za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wace ndi amace a iye wopenya;