John 9:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi ananena atate wace ndi amace, cifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu ali yense adzambvomereza iye kuti ndiye Kristu, akhale woletsedwa m'sunagoge,