John 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiŵiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziŵa kuti munthu amene uja ngwochimwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anamuitana kaciwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wocimwa.